Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 1:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufuma kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufumu kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono adamufunsa kuti, “Tatiwuza, masoka ameneŵa atigwera chifukwa cha yani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nkuti? Ndiwe mtundu wanji?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsono anamufunsa kuti, “Tatiwuze, tsoka limeneli latigwera chifukwa chiyani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nʼkuti? Ndiwe mtundu wanji wa anthu?”

Onani mutuwo Koperani




Yona 1:8
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.


Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.


Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa