Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pambuyo pake adabalanso Abele, mng'ono wa Kaini. Abele anali woŵeta nkhosa, koma Kaini anali mlimi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kenaka anabereka mʼbale wake Abele. Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 4:2
19 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta mu Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.


Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.


Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.


Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.


Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wampesa:


Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele.


kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;


kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa