Genesis 43:2 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono banja la Yakobe lija litadya tirigu yense amene adaakasuma ku Ejipito uja, Yakobe adauza ana ake aja kuti, “Pitaninso, mukatigulireko chakudya pang'ono.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono atatha kudya tirigu yense amene anakatenga ku Igupto, Yakobo anati kwa ana ake aja, “Pitani kuti mukatigulire chakudya china pangʼono.” |
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.