Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Genesis 42:4 - Buku Lopatulika Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe sadamtume nawo Benjamini, mng'ono wake weniweni wa Yosefe uja, chifukwa ankaopa kuti angapeze tsoka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yakobo sanamulole Benjamini mngʼono wake wa Yosefe kuti apite nawo chifukwa anaopa kuti choyipa chingamuchitikire. |
Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,
Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.
Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.
Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.