Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Genesis 42:3 - Buku Lopatulika Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu mu Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu m'Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero abale ake a Yosefe khumi adanyamuka kupita ku Ejipito kukagula tirigu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho abale ake khumi a Yosefe anapita kukagula tirigu ku Igupto. |
Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.
Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye.
Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.