ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;
Genesis 41:6 - Buku Lopatulika Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka padaphukanso ngala zina zisanu ndi ziŵiri zofwapa ndi zopserera ndi mphepo yamkuntho yakuvuma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka ngala zina zisanu ndi ziwiri zinaphuka. Izi zinali zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa. |
ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;
Ndipo anagona nalotanso kachiwiri; ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino.
Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota.
Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? Sudzauma chiumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? Udzauma pookedwa apo udaphuka.
Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.
Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.
Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.
Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.