Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
Genesis 40:18 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yosefe adamuyankha kuti, “Kamasulidwe kake ka maloto ameneŵa ndi aka: nsengwa zitatu ndi masiku atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. |
Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
m'lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'lichero la pamutu panga.
akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.
Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira.
Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto lili limodzi.
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.
ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.