Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 40:19 - Buku Lopatulika

19 akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, ndipo adzadula mutu wako. Tsono mtembo wako adzaupachika pa mtengo, ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 40:19
17 Mawu Ofanana  

akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.


m'lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'lichero la pamutu panga.


Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu;


Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake.


Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira.


Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika.


Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku.


Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.


Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.


Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo zakuthengo, akuyese chakudya.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.


Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapachika pa mitengo isanu; nalikupachikidwa pa mitengo mpaka madzulo.


Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mzinda; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.


Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa