Genesis 40:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Patangopitadi masiku atatu, padachitika phwando lokondwerera tsiku lobadwa Farao, ndipo Faraoyo adaitana nduna zake zonse. Tsono adamtulutsa uja woperekera vinyoyu pamodzi ndi wophika buledi yemwe uja. Aŵiri onse aja adaŵaimika pamaso pa nduna zake zija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. Onani mutuwo |
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;