ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
Genesis 40:10 - Buku Lopatulika ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa unali ndi nthambi zitatu. Masamba ake atangophukira, pomwepo panaoneka maluŵa, pambuyo pake panaonekanso mphesa zakupsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. |
ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.
Ndipo wopereka chikho wamkulu anafotokozera Yosefe loto lake, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga:
Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa.
Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n'kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n'kubereka akatungurume.