Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 17:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n'kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n'kubereka akatungurume.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nichita maluwa, nipatsa akatungurume.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 M'maŵa mwake Mose adakaloŵa m'chihema chaumboni. Adangoona ndodo ya Aroni, ya fuko la Levi, itaphuka masamba nkuchitanso maluŵa, ndipo itabala zipatso zakupsa za mtundu wa matowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 17:8
13 Mawu Ofanana  

ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha;


Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Ndipo mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.


Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.


Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.


nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.


Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.


Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake.


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa