Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.
Genesis 4:22 - Buku Lopatulika Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zila adabala Tubala-Kaini. Iyeyu ndiye kholo la onse ogwira ntchito yosula mkuŵa ndi zitsulo. Mlongo wa Tubala-Kainiyo anali Naama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama. |
Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.
Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine mu Yuda ndi mu Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.
Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa; ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.
dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yake nja chitsulo, ndi m'mapiri ake mukumbe mkuwa.