Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Genesis 4:19 - Buku Lopatulika Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lameki adakwatira akazi aŵiri. Dzina la mkazi wake woyamba linali Ada, la mkazi wachiŵiri linali Zila. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. |
Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki.
Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.