Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi;
Genesis 4:18 - Buku Lopatulika Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Enoki adabereka mwana namutcha Iradi. Iradi adabereka Mehuyaele. Mahuyaele adabereka Metusaele amene adabereka Lameki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki. |
Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi;
Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.
Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.
Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela:
Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameki;