Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Genesis 38:4 - Buku Lopatulika Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatenganso pena pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Onani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatenganso pathupi nabala mwana wa mwamuna ndipo anamutcha Onani. |
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.
Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.