Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Genesis 38:3 - Buku Lopatulika Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Ere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna amene anamutcha Eri. |
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.
Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.