Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.
Genesis 38:1 - Buku Lopatulika Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo Yuda adachoka nakakhala kwa munthu wina wa fuko la Adulamu dzina lake Hira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake napita kukakhala ndi munthu wina wa ku Adulamu wotchedwa Hira. |
Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.
Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole padzanja la mkazi; koma sanampeze iye.
Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.
Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.
Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.
Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m'hema, namfunda ndi chimbwi.
Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.