Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.
Genesis 27:44 - Buku Lopatulika ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka utamchokera ukali mkulu wako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka wamchokera ukali wa mkulu wako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bakakhala kwa iyeyo kanthaŵi ndithu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika. |
Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.
Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; nilidzatsikanso ngati mtsinje wa mu Ejipito;