Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:41 - Buku Lopatulika

41 Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Umu ndi m'mene zidaaliri zinthu pa zaka makumi aŵiri zomwe ndidakhala ndi inu. Ndidakugwirirani ntchito zaka khumi ndi zinai chifukwa cha ana anu aŵiriŵa, ndipo zaka zisanu ndi chimodzi ndidagwirira zoŵeta. Komabe malipiro anga mwakhala mukusintha kakhumi konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Zinthu zinali chonchi kwa zaka makumi awiri zimene ndinali mʼnyumba mwanu. Ndinakugwirirani ntchito kwa zaka khumi ndi zinayi chifukwa cha ana anu aakazi awiri ndipo zaka zina zisanu ndi chimodzi chifukwa cha ziweto zanu, ndipo munandisinthira malipiro kakhumi konse.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:41
12 Mawu Ofanana  

ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka utamchokera ukali mkulu wako;


Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?


Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.


Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.


Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga.


Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.


Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.


Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa