Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:40 - Buku Lopatulika

40 Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Nthaŵi zambiri ndinkavutika ndi kutentha masana ndiponso ndi kuzizira usiku. Sindinkatha kuwona tulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Moyo wanga unali wotere: Dzuwa limanditentha masana ndipo usiku ndimazunzika ndi kuzizira. Tulo sindimalipeza konse.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:40
13 Mawu Ofanana  

Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.


Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku.


Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.


Ndipo ndinaitana chilala chidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi ntchito zonse za manja.


Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.


amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;


Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa