Genesis 27:34 - Buku Lopatulika Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!” |
Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang'amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mzinda, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa,
Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.
Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.