Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.
Genesis 27:16 - Buku Lopatulika ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamuvekanso zikopa za tianatambuzi pamikono pake ndiponso pakhosi pake posalala popanda cheya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi. |
Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.
Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono;
ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga.
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.