Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 25:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Mwana woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala chaubweya. Motero adamutcha Esau.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:25
10 Mawu Ofanana  

Atatha masiku ake akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwake.


Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.


Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala.


ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala;


Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.


Ndipo Abrahamu anabala Isaki. Ana a Isaki: Esau, ndi Israele.


Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;


Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;


Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.


Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa