Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa.
Genesis 25:3 - Buku Lopatulika Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yokisani adabereka Sheba ndi Dedani, ndipo ana a Dedani anali Aasuri, Aletusi ndi Aleumi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. |
Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa.
Ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.
namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.
Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.
Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.
Katundu wa pa Arabiya. M'nkhalango ya mu Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.
Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.
Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala mu Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.
Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.
Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.