Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 2:9 - Buku Lopatulika

9 namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono adamlonga ufumu kuti akhale mfumu ya Giliyadi, Asere, Yezireele, Efuremu ndi Benjamini, kungoti Israele yense.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:9
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.


Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.


Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo.


Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo.


Ndi a ana a Efuremu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.


Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.


A ana a Asere, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda;


Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao;


pamodzi ndi mizinda adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, mizinda yonse pamodzi ndi midzi yao.


Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.


Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.


Ndipo malire ake mbali ya kum'mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao.


Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu;


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.


koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse.


Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa