Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Genesis 23:12 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Abrahamu adaŵerama pamaso pa anthu onse aja, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Apo Abrahamu anaweramanso mwaulemu pamaso pa anthu a mʼdzikolo |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.
Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.