Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.
Genesis 22:6 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m'manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, |
Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.
Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.
ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa mu Chihebri, Gologota:
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.