Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.” Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:6
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri.


Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.


Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele.


Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.


Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordani, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordani asefuka m'magombe ake onse, nyengo yonse ya masika,


Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.


Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;


Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa