Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:17 - Buku Lopatulika

17 ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa mu Chihebri, Gologota:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa m'Chihebri, Gologota:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota.”)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa “Malo a Bade” (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota).

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:17
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri.


Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mzinda, namponya miyala, namupha.


Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.


Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.


Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.


Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.


Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.


Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.


Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.


Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.


Ndipo pamene anafika kumalo dzina lake Bade, anampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi ochita zoipa omwe, mmodzi kudzanja lamanja ndi wina kulamanzere.


Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.


Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.


Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma mu Chihebri, Gabata.


Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa