Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
Genesis 2:6 - Buku Lopatulika koma inakwera nkhungu yotuluka padziko lapansi, nkuthirira ponse pamwamba panthaka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma inakwera nkhungu yotuluka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma madzi ankatuluka m'dziko lonse lapansi ndi kumathirira nthaka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma kasupe ankatuluka mʼnthaka ndi kuthirira pa dziko lonse. |
Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.