Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.
Genesis 2:15 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira. |
Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.
Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.
Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.
Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga;
Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.