Genesis 2:13 - Buku Lopatulika Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Kusi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni; uwu umazungulira dziko lonse la Kusi. |
Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;
Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.