Genesis 19:4 - Buku Lopatulika Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alendowo asanakagone, anthu onse amumzindamo, achinyamata ndi okalamba omwe, adadzazinga nyumbayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti. |
Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu,
Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu;
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.
Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mzindawo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.