Genesis 19:2 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.” |
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.
Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.
Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.
Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.
Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji? Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenji?
Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.
Pomwepo anathira madzi m'beseni, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.