Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Genesis 15:7 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anamuwuza kuti, “Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.” |
Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.
ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu.
Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwe kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.
Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.
Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.