Genesis 14:9 - Buku Lopatulika ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kumenyana ndi asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi Kedorilaomere wa ku Elamu, Tidala wa ku Goimu, Amurafere wa ku Sinara ndi Ariyoki wa ku Elasara, mafumu asanu kulimbana ndi mafumu anai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. |
Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari) ndipo anawathira nkhondo m'chigwa cha Sidimu;
Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,