Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 14:12 - Buku Lopatulika

Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala mu Sodomu, ndi chuma chake, namuka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi chuma chake, namuka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adamtenganso Loti, mphwake wa Abramu uja, pamodzi ndi zake zonse, chifukwa ankakhala ku Sodomu komweko.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anatenganso Loti, mwana wa mʼbale wake wa Abramu pamodzi ndi katundu wake popeza ankakhala mu Sodomu.

Onani mutuwo



Genesis 14:12
13 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.


Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.


Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.


Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.


Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.


Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.


Mkwapulo ukapha modzidzimutsa, adzaseka tsoka la wosachimwa.


Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.