Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 18:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati, “Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo, kuti mungachimwire nawo pamodzi, miliri yao ingakugwereniko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti: “ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’ mungachimwe naye kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 18:4
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.


Pakuona mbala, uvomerezana nayo, nuchita nao achigololo.


Tulukani inu mu Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.


Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.


Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m'dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.


Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.


Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu musaime chiimire; mukumbukire Yehova kutali, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu.


Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.


Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.


ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa