Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Genesis 14:11 - Buku Lopatulika Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mafumu anai aja adatenga zonse za ku Sodomu ndi za ku Gomora, pamodzi ndi chakudya, nachokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo. |
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.
Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.
Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.
ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.