Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Genesis 13:5 - Buku Lopatulika Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Loti nayenso amene ankayenda limodzi ndi Abramu, anali ndi nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe pamodzi ndi banja lake ndi antchito ake amene ankakhala naye limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Loti amene ankayendayenda ndi Abramu nayenso anali ndi ziweto zosiyanasiyana ndi matenti. |
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.
Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zotchingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse.