Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Genesis 13:11 - Buku Lopatulika Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Loti anadzisankhira yekha chigwa chonse cha Yorodani nanyamuka kulowera cha kummawa. Choncho anthu awiriwa anasiyana. |
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'mizinda ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.
Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo:
Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.
Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.
osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.