Genesis 11:16 - Buku Lopatulika Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Eberi ali wa zaka 34, adabereka mwana dzina lake Pelegi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. |
Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.
ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Ndi Eberi anabala ana aamuna awiri, dzina la winayo ndiye Pelegi, popeza masiku ake dziko linagawanika; ndi dzina la mbale wake ndiye Yokotani.
Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka.