Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Genesis 11:11 - Buku Lopatulika ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 500, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri;
Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.