zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Genesis 1:19 - Buku Lopatulika Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachinai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi. |
zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga.
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.
Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.