ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
Genesis 1:17 - Buku Lopatulika Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi, |
ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao;
Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;
Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.