Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
Filemoni 1:15 - Buku Lopatulika Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kapena Onesimo adangokusiya kanthaŵi pang'ono, kuti udzakhale naye nthaŵi zonse, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. |
Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?