Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 9:24 - Buku Lopatulika

Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo panali mvula yamatalala ndi mphezi zong'anima kwambiri. Matalala ake anali oopsa kwambiri, kotero kuti chiyambire pamene Aejipito adasanduka mtundu wa anthu oima paokha, matalala otere sadagwepo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha.

Onani mutuwo



Eksodo 9:24
11 Mawu Ofanana  

amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo?


Anawapatsa mvula yamatalala, lawi la moto m'dziko lao.


Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.


ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.


Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.


Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala padziko la Ejipito.


Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse zakuthengo, nathyola mitengo yonse yakuthengo.


Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.


Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m'mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m'kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m'kati mwa moto.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho mu ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala aakulu adzalitha mu ukali wanga.


pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.