Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?
koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;
Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.
Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.