Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 9:13 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mammawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo Chauta adauza Mose kuti, “Maŵa m'mamaŵa upite ukakumane ndi Farao, ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze.

Onani mutuwo



Eksodo 9:13
5 Mawu Ofanana  

Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.


Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.


Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.


Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.


Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire,