Eksodo 8:24 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto. |
Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.
Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.